Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 13:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.

12. Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.

13. Ndipo cicita zizindikilo zazikuru, kutinso citsitse moto ucokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.

14. Ndipo cisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikilo zimene anacipatsa mphamvu yakuzicita pamaso pa cirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fane la ciromboco, cimene cinali nalo bala la lupanga nicinakhalanso ndi moyo.

15. Ndipo anacipatsa mphamvu yakupatsa fano la cirombo mpweya, kutinso fane la cirombo Iilankhule, nilicite kuti onse osalilambira fane la cirombo aphedwe.

16. Ndipo cicita kuti onse, ang'ono ndi akuru, acuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire cilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao;

17. ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala naco cilembo, ndilo dzina la cirombo, kapena ciwerengero ca dzina lace.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 13