Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 12:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo cizindikilo cacikuru cinaoneka m'mwamba; mkazi wobvekedwa dzuwa, ndi mwezi ku mapazi ace, ndi pamutu pace korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;

2. ndipo anali ndi pakati; ndipo apfuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.

3. Ndipo cinaoneka cizindikilo cina m'mwamba, taonani, cinjoka cofiira, cacikuru, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pace nduwira zacifumu zisanu ndi ziwiri.

4. Ndipo mcira wace uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo cinjoka cinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala, ico cikalikwire mwana wace.

5. Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wace amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wacifumu wace.

6. Ndipo mkazi anathawira kucipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

7. Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikayeli ndi angelo ace akucita nkhondo ndi cinjoka; cinjokanso ndi angelo ace cinacita nkhondo;

8. ndipo sicinalakika, ndipo sanapezekanso malo ao m'mwamba.

9. Ndipo cinaponyedwa pansi cinjoka cacikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; cinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 12