Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 10:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. nalumbira kuchula iye amene ali ndi moyo ku nthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:

7. komatu m'masiku a mau a mngelo wacisanu ndi ciwiri m'mene iye adzayamba kuomba, pamenepo padzatsirizika cinsinsi ca Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ace aneneri.

8. Ndipo mau ndinawamva ocokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalom'dzanja la mngelo wakuimirira panyanja ndi padziko.

9. Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimbamwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uci.

10. Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uci; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.

11. Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 10