Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 8:3-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita, popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo m'thupi;

4. kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.

5. Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:

6. pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.

7. Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero.

8. Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.

9. Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu.

10. Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.

11. Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.

12. Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi;

13. pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za thupi, mudzakhala ndi moyo.

14. Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu,

15. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,

16. Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;

17. ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.

18. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

Werengani mutu wathunthu Aroma 8