Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 8:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,

16. Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu;

17. ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.

18. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

19. Pakuti ciyembekezetso ca colengedwa cilimilia bvumbulutso la ana a Molungu.

20. Pakuti colengedwaco cagonietsedwa kuutsiru, cosafuna mwini, koma cifukwa ca iye amene anacigonjetsa,

21. ndi ciyembekezo kuti colengedwa comwe cidzamasulidwa ku ukapolo wa cibvundi, ndi kolowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu,

22. Pakuti tidziwa kuti colengedwa conse cibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.

23. Ndipo si cotero cokha, koma ife tomwe, tiri nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo ciomboledwe ca thupi lathu.

Werengani mutu wathunthu Aroma 8