Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 6:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti pakufa iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

11. Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.

12. Cifukwa cace musamalola ucimo ucite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zace:

13. ndipo musapereke ziwalo zanu kuucimo, zikhale zida za cosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo ataturuka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za cilungamo,

14. Pakuti ucimo sudzacita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a cisomo.

15. Ndipo ciani tsono? Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri a lamulo, koma a cisomo? Msatero ai.

16. Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kucilungamo?

17. Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco;

18. ndipo pamene munamasulidwa kuucimo, munakhala akapolo a cilungamo,

19. Ndilankhula manenedwe a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa ndi a kusayeruzika kuti zicite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a cilungamo kuti zicite ciyeretso.

20. Pakuti pamene inu munali aka polo a ucimo, munali osatumikira cilungamo.

21. Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu izi ciri imfa.

22. Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuucimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli naco cobala canu cakufikira ciyeretso, ndi cimariziro cace moyo wosatha.

Werengani mutu wathunthu Aroma 6