Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 3:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo potero Myuda aposa Dinji? Kapena mdulidwe upindulanji?

2. Zambiri monse monse: coyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo.

3. Nanga bwanji ngati ena sanakhulupira? Kodi kusakhulupira kwao kuyesa cabe cikhulupiriko ca Mulungu?

4. Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa,Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu,Ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa.

5. Koma ngati cosalungama cathu citsimikiza cilungamo ca Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (ndilankhula umo anenera munthu).

6. Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi?

7. Pakuti ngati coonadi ca Mulungu cicurukitsa ulemerero wacecifukwa ca bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wocimwa?

8. Ndipo tilekerenji kunena, Ticite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.

Werengani mutu wathunthu Aroma 3