Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 10:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. kapena, Adzatsikira ndani kudzenieko? ndiko, kukweza Kristu kwa akufa.

8. Koma citani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a cikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:

9. kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:

10. pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi m'kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso

11. Pakuti lembo litere, Amene ali yense akhulupirira iye, sadzacita manyazi.

12. Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawacitira zolemera onse amene aitana pa iye;

13. pakuti, amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

14. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?

15. ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.

16. Koma sanamvera Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife?

17. Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.

18. Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu,Liu lao linaturukira ku dziko lonse lapansi,Ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.

Werengani mutu wathunthu Aroma 10