Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 10:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?

15. ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.

16. Koma sanamvera Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife?

17. Comweco cikhulupiriro cidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Kristu.

18. Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu,Liu lao linaturukira ku dziko lonse lapansi,Ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.

19. Koma nditi, Kodi Israyeli alibe kudziwa? Poyamba Mose anena,Ine ndidzacititsa inu nsanje ndi iwo amene sakhala mtundu wa anthu,Ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.

20. Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati,Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifuna;Ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunsa.

21. Koma kwa Israyeli anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana.

Werengani mutu wathunthu Aroma 10