Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 1:8-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Kristu cifukwa ca inu nonse, cifukwa kuti mbiri ya cikhulupiriro canu idamveka pa dziko lonse lapansi.

9. Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, m'Uthenga Wabwino wa Mwana wace, kuti kosalekeza ndikumbukila inu, ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga,

10. ngati nkutheka tsopano mwa cifuniro ca Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu.

11. Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;

12. ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa cikhulupiriro ca ife tonse awiri, canu ndi canga.

13. Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawiri kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.

14. Ine ndiri wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.

15. Cotero, momwe ndingakhoze ine, ndirikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma.

16. Pakuti Uthenga Wabwino sundicititsa manyazi; pakuti uti mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.

17. Pakuti m'menemo caonetsedwa cilungamoca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro.

18. Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wocokera Kumwamba, uonekera pa cisapembedzo conse ndi cosalungama ca anthu, amene akanikiza pansi coonadi m'cosalungama cao;

19. cifukwa codziwika ca Mulungu caonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anacionetsera kwa iwo.

20. Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;

Werengani mutu wathunthu Aroma 1