Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aroma 1:16-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pakuti Uthenga Wabwino sundicititsa manyazi; pakuti uti mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.

17. Pakuti m'menemo caonetsedwa cilungamoca Mulungu cakucokera kucikhulupiriro kuloza kucikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro.

18. Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wocokera Kumwamba, uonekera pa cisapembedzo conse ndi cosalungama ca anthu, amene akanikiza pansi coonadi m'cosalungama cao;

19. cifukwa codziwika ca Mulungu caonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anacionetsera kwa iwo.

20. Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;

21. cifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamcitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pace m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira,

22. Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;

23. nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi cifaniziro ca munthu woonongeka ndi ca mbalame, ndi ca nyama zoyendayenda, ndi ca zokwawa.

24. Cifukwa cace Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kucititsana matupi ao wina ndi mnzace zamanyazi;

25. amenewo anasandutsa coonadi ca Mulungu cabodza napembedza, natumikira colengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.

26. Cifukwa ca ici Mulungu anawapereka iwo 1 ku zilakolako za manyazi; pakuti angakhale akazi ao anasandutsa macitidwe ao a cibadwidwe akhale macitidwe osalingana ndi cibadwidwe:

27. ndipo cimodzimodzinso amuna anasiya macitidwe a cibadwidwe ca akazi, natenthetsana ndi colakalaka cao wina ndi mnzace, amuna okhaokha anacitirana camanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.

28. Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'cidziwitso cao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukacita zinthu zosayenera;

29. anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, cinyengo, udani;

30. akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, acipongwe, odzitama, amatukutuku, ovamba zoipa, osamvera akuru ao,

31. opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda cikondi ca cibadwidwe, opanda cifundo;

32. amene ngakhale adziwa kuweruza kwace kwa Mulungu, kuti iwo 2 amene acita zotere ayenera imfa, azicita iwo okha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzicita.

Werengani mutu wathunthu Aroma 1