Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Akolose 1:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. cifukwa ca ciyembekezo cosungikira kwa inu m'Mwamba, cimene mudacimva kale m'mau a coonadi ca Uthenga Wabwino,

6. umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu; kuyambira tsikulo mudamva nimunazindildra cisomo ca Mulungu m'coonadi;

7. monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiyemtumiki wokhulupirika wa Kristu cifukwa ca ife;

8. amenenso anatifotokozera cikondi canu mwa Mzimu.

9. Mwa ici ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi cizindikiritso ca cifuniro cace mu nzeru zonse ndi cidziwitso ca mzimu,

10. kuti mukayende koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu nchito yonse yabwino, ndi kukula m'cizindikiritso ca Mulungu;

11. olimbikitsidwa m'cilimbiko conse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wace, kucitira cipiriro conse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi cimwemwe,

12. ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao colowa ca oyera mtima m'kuunika;

13. amene anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa cikondi cace;

14. amene tiri nao maomboledwe mwa iye, m'kukhululukidwa kwa zocimwa zathu;

15. amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse;

16. pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.

17. Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye.

18. Ndipo iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo; ndiye ciyambi, wobadwa woyamba woturuka mwa akufa; kuti akakhale iye mwa zonse woyambayamba.

Werengani mutu wathunthu Akolose 1