Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 8:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Losati longa pangano ndinalicita ndi makolo ao,Tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera aturuke m'dziko la Aigupto;Kuti iwo sanakhalabe m'pangano langa,Ndipo loe sindinawasamalira iwo, anena Ambuye,

10. Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israyeli,Atapita masiku ajawa, anena Ambuye:Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao,Ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo;Ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu,Ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:

11. Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzace,Ndipo yense mbale wace, ndi kuti, Zindikira Ambuye:Pakuti onse adzadziwa Ine, Kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru wa iwo.

12. Kuti ndidzacitira cifundo rosalungama zao,Ndipo zoipa zao sindidzazikumbukanso.

13. Pakunena iye, Latsopano, anagugitsa loyambali. Koma cimene cirimkuguga ndi kusukuluka, cayandikira kukanganuka.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 8