Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 6:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu ziri zoposa ndi zophatikana cipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;

10. pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

11. Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere cangu comweci colinga ku ciyembekezo cokwanira kufikira citsiriziro;

12. kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa cikhulupiriro ndi kuleza mtima.

13. Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkuru woposa kumlumbira, analumbira pa iye yekha,

14. nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kucurukitsa ndidzakucurukitsa iwe.

15. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.

16. Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'citsutsano cao ciri conse lumbiro litsiriza kutsimikiza.

17. Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mocurukira kwa olowa a lonjezano kuti cifuniro cace sicisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;

18. kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale naco coticenjeza colimba, ife amene tidathawira kucigwira ciyembekezo coikika pamaso pathu;

Werengani mutu wathunthu Ahebri 6