Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 6:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwa ici, polekana nao mau a ciyambidwe ca Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo nchito zakufa, ndi a cikhulupiriro ca pa Mulungu,

2. a ciphunzitso ca ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a ciweruziro cosatha.

3. Ndipo ici tidzacita, akatilola Mulungu.

4. Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yace, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,

5. nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi irinkudza,

6. koma anagwa m'cisokero; popeza adzipaeikiranso okha Mwana wa Mulungu, namcititsa manyazi poyera.

7. Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawiri kawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso locokera kwa Mulungu:

8. koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; citsiriziro cace ndico kutenthedwa.

9. Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu ziri zoposa ndi zophatikana cipulumutso, tingakhale titero pakulankhula;

10. pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala nchito yanu, ndi cikondico mudacionetsera ku dzina lace, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 6