Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 12:16-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. kuti pangakhale wacigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wace wobadwa nao mtanda umodzi wa cakudya.

17. Pakutf mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeza malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.

18. Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsya moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe,

19. ndi mau a lipenga, ndi maaenedwe a mau, manenedweamene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau;

20. pakuti sanakhoza kulola colamulidwaco. Ingakhale nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala;

21. ndipo maonekedwewo anali oopsa otere, kuti Mose anati, Ndiopatu ndi kunthunthumira.

22. Komatu mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wocuruka wa angelo,

23. ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro,

24. ndi kwa Yesu Nkhoswe ya cipangano catsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula cokoma coposa mwazi wa Abeli.

25. Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuka, pomkana iye amene anawacenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa iye wa Kumwamba;

26. amene mau ace anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.

27. Ndipo ici, cakuti kamodzinso, cilozera kusuntha kwace kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.

28. Mwa ici polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale naco cisomo, cimene tikatumikire naco Mulungu momkondweretsa, ndi kumcitira ulemu ndi mantha.

29. Pakuti 1 Mulungu wathu ndiye mota wonyeketsa.

Werengani mutu wathunthu Ahebri 12