Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ahebri 1:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iri yonse,Iwe ndiwe Mwana wanga,Lero ine ndakubala Iwe?ndiponso,Ine ndidzakhala kwa iye Atate,Ndipo iye adzakhala kwa ine Mwana?

6. Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire iye angelo onse a Mulungu.

7. Ndipo za angelo anenadi,Amene ayesa angelo ace mizimu,Ndi omtumikira iye akhale lawi lamoto;

8. Koma ponena za Mwana, ati,Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi;Ndipo ndodo yacifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.

9. Mwakonda cilungamo, ndi kudana naco coipa;Mwa ici Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozaniNdi mafuta a cikondwerero ceni ceni koposa anzanu.

10. Ndipo,Inu, Ambuye, paciyambipo munaika maziko ace a dziko,Ndipo miyamba iri nchito ya manja anu;

Werengani mutu wathunthu Ahebri 1