Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 6:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, cocokera m'thupi adzatuta cibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, cocokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

9. Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.

10. Cifukwa cace, monga tiri nayo nyengo, ticitire onse cokoma, koma makamaka iwo a pa banja la cikhulupiriro.

11. Taonani, malembedwe akuruwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.

12. Onseamene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukangamizani inu mudulidwe; cokhaco, cakuti angazunzike cifukwa ca mtanda wa Kristu.

13. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu.

14. Koma kudzitamandira ine konse konse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene mwa iye dziko lapansi lapacikidwira ine, ndi ine ndapacikidwira dziko lapansi.

15. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwakulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 6