Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 6:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa cifatso; ndikudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

2. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse cilamulo ca Kristu.

3. Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali cabe, adzinyenga yekha.

4. Koma yense ayesere nchito yace ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira cifukwa ca iye yekha, si cifukwa ca wina,

5. Pakuti yense adzasenza katundu wace wa iye mwini.

6. Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kucereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.

7. Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti cimene munthu acifesa, cimenenso adzacituta.

8. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, cocokera m'thupi adzatuta cibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, cocokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

9. Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.

10. Cifukwa cace, monga tiri nayo nyengo, ticitire onse cokoma, koma makamaka iwo a pa banja la cikhulupiriro.

11. Taonani, malembedwe akuruwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 6