Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 5:7-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere coonadi?

8. Kukopa kumene sikucokera kwa iye anakuitanani.

9. Cotupitsa pang'ono citupitsa mtanda wonse.

10. Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakubvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza citsutso cace.

11. Koma ine, abale, ngati ndilalikiransoindulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo cikhumudwitso ca mtanda cidatha.

12. Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.

13. Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; cokhaco musacite nao ufulu wanu cothandizira thupi, komatu mwa cikondi citiranani ukapolo.

14. Pakuti mau amodzi akwaniritsa cilamulo conse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

15. Koma ngati mulumana ndi kudyana, cenjerani mungaonongane.

16. Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.

17. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.

18. Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.

19. Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano,

20. nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru,

21. kuledzera, mcezo, ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

22. Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro,

23. cifatso, ciletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

24. Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba zace, ndi zilakolako zace.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 5