Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Agalatiya 2:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Kristu, tipezedwanso tiri ocimwa tokha, kodi Kristu ali mtumikiwa ucimo cifukwa cace? Msatero ai.

18. Pakuti ngati izi zomwezi ndazigumula ndizimanganso, ndidzitsimikizira ndekha ndirt wolakwa.

19. Pakuti ine mwa lamulo ndafa ku lamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.

20. Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi mayo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao: tsopano m'thupi, ndiri nao m'cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.

21. Sindieiyesa copanda pace cisomo ca Mulungu; pakuti ngati cilungamo ciri mwa Lamulo, Kristu adafa cabe.

Werengani mutu wathunthu Agalatiya 2