Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Aefeso 2:6-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Kristu Yesu;

7. kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu.

8. Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;

9. cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense.

10. Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

11. Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, ochedwa kusadulidwa ndi iwo ochedwa mdulidwe m'thupi, umene udacitika ndi manja;

12. kuti nthawi ija munali opanda Kristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda ciyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.

13. Koma tsopano mwa Yesu Kristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Kristu.

14. Pakuti iye ndiye mtendere wathu, amene anacita kutionse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,

15. atacotsa udani m'thupi lace, ndiwo mau a cilamulo ca kuchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kucitapo mtendere;

16. ndi kuti akayanianitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo;

17. ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;

18. kuti mwa iye ife tonse awiri tiri nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi.

19. Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;

Werengani mutu wathunthu Aefeso 2