Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Yohane 1:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira paciyambi, kuti tikondane wina ndi mnzace.

6. Ndipo cikondi ndi ici, kuti tiyende monga mwa malamulo ace. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira paciyambi, kuti mukayende momwemo.

7. Pakuti onyenga ambiri adaturuka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene sabvomereza kuti Yesu Kristu anadza m'thupi, Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Kristu.

8. Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazicita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.

9. Yense wakupitirira, wosakhala m'ciphunzitso ca Kristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m'ciphunzitso, iyeyo ali nao Arate ndi Mwana.

10. Munthu akadza kwa inu, wosatenga ciphunzitso ici, musamlandire iye kunyumba, ndipo musamlankhule.

11. Pakuti iye wakumlankhula ayanjana nazo nchito zace zoipa.

12. Pokhala ndiri nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kucita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti cimwemwecanucikwanire.

13. Akulankhulani ana a mbale wanu wosankhika.

Werengani mutu wathunthu 2 Yohane 1