Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Timoteo 4:8-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. cotsalira wandiikira ine korona wa cilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ace.

9. Tayesetsa kudza kwa ine msanga:

10. pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalimatiya.

11. Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira.

12. Koma Tukiko ndamtuma ku Efeso.

13. Copfunda cija ndinacisiya ku Trowa kwa Karpo, udze naco pakudza iwe, ndi mabuku, makamaka zikopa zija zolembedwa.

14. Alesandro wosula mkuwa anandicitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa nchito zace;

15. ameneyo iwenso ucenjere naye; pakuti anatsutsana nao mau athu.

16. Pa codzikanira canga coyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; cimeneco cisawerengedwe cowatsutsa.

17. Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine cilalikiro cimveke konse konse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.

18. Ambuye adzandilanditsa ku nchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wace wa Kumwamba; kwa iye ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.

19. Lankhula Priska ndi Akula, ndi banja la Onesiforo.

Werengani mutu wathunthu 2 Timoteo 4