Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Timoteo 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO a mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Kristu Yesu,

2. kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Ambuye wathu.

3. Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi cikumbu mtima coyera, kuti ndikumbukila iwe kosalekeza m'mapemphero anga,

4. pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukila misozi yako, kuti ndidzazidwe naco cimwemwe;

5. pokumbukila cikhulupiriro cosanyenga ciri mwa iwe, cimene cinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunike, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.

6. Cifukwa cace ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, iri mwa iwe mwa kuika kwa manja anga,

7. Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.

Werengani mutu wathunthu 2 Timoteo 1