Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Petro 3:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti ici aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;

6. mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;

7. koma miyamba ndi dziko lamasiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la ciweruzo ndi cionongeko ca anthu osapembedza.

8. Koma ici cimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka cikwi, ndi zaka cikwi ngati tsiku limodzi.

9. Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena aciyesa cizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

10. Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi cibumo cacikuru, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kurentha kwakukuru, ndipo dziko ndi nchito ziri momwemo zidzarenthedwa.

11. Popezaizi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'cipembedzo,

12. akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwace kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha mota idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukuru.

Werengani mutu wathunthu 2 Petro 3