Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi cibumo cacikuru, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kurentha kwakukuru, ndipo dziko ndi nchito ziri momwemo zidzarenthedwa.