Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Atesalonika 2:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;

3. munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma ciyambe cifike cipatukoco, nabvumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa cionongeko,

4. amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zochedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhalapansi ku Kacisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.

5. Simukumbukila kodi, kuti pokhala nanu, ndisanacoke ine, ndinakuuzani izi?

6. Ndipo tsopano comletsa mucidziwa, kuti akabvumbulutsidwe iye m'nyengo yace ya iye yekha.

Werengani mutu wathunthu 2 Atesalonika 2