Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Atesalonika 2:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo tikupemphani, abale, cifukwa ca kudza kwace kwa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa iye;

2. kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;

3. munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma ciyambe cifike cipatukoco, nabvumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa cionongeko,

4. amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zochedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhalapansi ku Kacisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.

Werengani mutu wathunthu 2 Atesalonika 2