Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Atesalonika 1:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu, abale, monga kuyenera; pakuti cikhulupiriro canu cikula cikulire, ndipo cicurukira cikondanoca inu nonse, yense pa mnzace;

4. kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m'Mipingo ya Mulungu, cifukwa ca cipiriro canu, ndi cikhulupiriro canu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;

5. ndico citsimikizo ca ciweruziro colungama ca Mulungu; kuti mu-kawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa;

6. popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera cisautso kwa iwo akucitira inu cisautso,

7. ndi kwa inu akumva cisautso mpumulo pamodzi ndi ire, pa bvumbulutso la Ambuye Yesu wocokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yace,

8. m'lawi lamoto, ndi kubwezera cilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;

Werengani mutu wathunthu 2 Atesalonika 1