Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 5:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tiri naco cimango ca kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba.

2. Pakutinso m'menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kubvekedwa ndi cokhalamo cathu cocokera Kumwamba;

3. ngatitu pobvekedwa sitidzapezedwa amarisece.

4. Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kubvulidwa, koma kubvekedwa, kuti caimfaco cimezedwe ndi moyo.

5. Ndipo wotikonzera ife ici cimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife cikhole ca Mzimu,

6. Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tiri kwathu m'thupi, sitiri kwa Ambuye,

7. (pakuti tiyendayenda mwa cikhulupiriro si mwa cionekedwe);

8. koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m'thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.

9. Cifukwa cacenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa iye.

10. Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa ku mpando wa kuweruza wa Kristu, kuti yense alandire zocitika m'thupi, monga momwe anacita, kapena cabwino kapena coipa.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 5