Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 4:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu,

8. iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.

9. Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.

10. Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu.

11. Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo

12. Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife;

13. m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, cifukwa anatipatsako Mzimu wace.

14. Ndipo ife tapenyera, ndipo ticita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.

15. Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 4