Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 4:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uli wonse, koma yesani mizimu ngati icokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anaturuka kulowa m'dziko lapansi.

2. M'menemo muzindikira Mzimu Wl Mulungu: mzimu uli wonse umen ubvomereza kuti Yesu Kristu ana dza m'thupi, ucokera mwa. Mulungu

3. ndipo mzimu uli wonse umen subvomereza Yesu sucokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzirm wa wokana Kristu umene mudamvi kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,

4. Inu ndinu ocokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti iye wakukhah mwa inu aposa iye wakukhala m'dzi ko lapansi. Iwo ndiwo ocoken m'dziko lapansi;

5. mwa ici alankhula monga ocokera m'dziko lapansi, ndipo dziko tapansi liwamve ra.

6. Ife ndife ocokera mwa Mu lungu; iye amene azindikira Mu lungu atimvera; iye wosacoken mwa Mulungu satimvera ife. Mo mwemo tizindikira mzimu wa coonadi, ndi mzimu wa cisokeretso.

7. Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu,

8. iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.

9. Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.

10. Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 4