Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 2:2-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. ndipo iye ndiye ciombolo ca macimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.

3. Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira iye, ngati tisunga malamulo ace.

4. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa iye, koma wosasunga malamulo ace, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe coonadi;

5. koma iye amene akasunga mau ace, mwa iyeyu zedi cikondi ca Mulungu cathedwa. M'menemo tizindikira kuti tiri mwa iye;

6. iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wace kuyenda monga anayenda Iyeyo.

7. Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa ciyambi; Lamulo Iakaielo ndilo mau amene mudawamva.

8. Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndico cimene ciri coona mwa iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala,

9. iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wace, ali mumdima kufikira tsopane lino.

10. Iye amene akonda mbale wace akhala m'kuunika, ndipo mwa iye mulibe cokhumudwitsa.

11. Koma iye wakumuda mbale wace ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ace.

12. Ndikulemberani, tiana, popeza macimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lace.

13. Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira iye amene ali kuyambir paciyambi. Ndikulemberani anyamata, popeza mwamlaka woipavo, Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

14. Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira iye amene ali kuyambira paciyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muti amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo.

15. Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko apansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, cikondi ca Atate lsiciri mwa iye.

16. Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.

17. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi cilakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 2