Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 6:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma cipembedzo pamodzi ndi kudekha cipindulitsa kwakukuru;

7. pakuti sitinatenga kanthu polowa m'dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pocoka pano;

8. koma pokhala nazo zakudya ndizopfunda, zimenezi zitikwanire.

9. Koma iwo akufuna kukhala acuma amagwa m'ciyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'cionongekondi citayiko.

10. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo cikondi ca pa ndalama; cimene ena pocikhumba, anasocera, nataya cikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.

11. Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate cilungamo, cipembedzo, cikhulupiriro, cikondi, cipiriro, cifatso.

12. Limba nayo nkhondo yabwino ya cikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wabvomereza cibvomerezo cabwino pamaso pa mboni zambiri.

13. Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Kristu Yesu, amene anacitira umboni cibvomerezo cabwino kwa Pontiyo Pilato;

14. kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda cirema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu;

15. limene adzalionetsa m'nyengo za iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye;

16. amene iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona; kwa iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.

17. Lamulira iwo acuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere cuma cosadziwika kukhala kwace, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kocurukira, kuti tikondwere nazo;

18. kuti acite zabwino, naeuruke ndi nchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 6