Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 1:3-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa cifundo cace cacikuru, anatibalanso ku ciyembekezo ca moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu;

4. kuti tilandire colowa cosabvunda ndi cosadetsa ndi cosafota, cosungikira m'Mwamba inu,

5. amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa cikhulupiriro, kufikira cipulumutso cokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza.

6. M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukacitidwe cisoni ndi mayesero a mitundu mitundu,

7. kuti mayesedwe a cikhulupiriro canu, ndiwo a mtengo wace woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ocitira ciyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu, Kristu;

8. amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi, cimwemwe cosaneneka, ndi ca ulemerero:

9. ndi kulandira citsiriziro ca cikhulupiriro canu, ndico cipulumutso ca moyo wanu.

10. Kunena za cipulumutso ici anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za cisomo cikudzerani;

11. ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo analozera, pakucitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero, worsarana nao.

12. Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kucokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.

13. Mwa ici, podzimanga m'cuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konse konse cisomo cirikutengedwa kudza naco kwa inu m'bvumbulutso la Yesu Kristu;

14. monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;

15. komatu monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse;

16. popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

17. Ndipo mukamuitana ngati Alate, iye amene aweruza monga mwa nchito ya yense, wopanda tsankhu, khalani ndi mantha nthawi ya cilendo canu;

18. podziwa kuti simunaomboledwa ndi zobvunda, golidi ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu acabe ocokera kwa makolo anu:

19. koma 1 ndi mwazi wa mtengo wace wapatali 2 monga wa mwana wa nkhosa wopanda cirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu:

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 1