Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 8:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti ngakhalenso iriko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iriko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri;

6. koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zicokera kwa iye, ndi ire kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse ziri mwa iye, ndi ife mwa iye.

7. Komatu cidziwitso siciri mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo cikumbu mtima cao, popeza ncofoka, cidetsedwa.

8. Koma cakudya sicitibvomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tiribe kupindulako,

9. Koma yang'anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale cokhumudwitsa ofokawo.

10. Pakuti wina akaona iwe amene uli naco cidziwitso, ulikukhala pacakudya m'kacisi wa fano, kodi cikumbu mtima cace, popeza ali wofoka, sieidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?

11. Pakuti mwa cidziwitso cako wofokayo atayika, ndiye mbale amene Kristu anamfera.

12. Koma pakucimwira abale, ndi kulasa cikumbu mtima cao cofoka, mucimwira kotero Kristu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 8