Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:29-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Koma ici nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;

30. ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;

31. ndi iwo akucita nalo dziko lapansi, monga ngati osacititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.

32. Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye;

33. koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wace.

34. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso iye wosakwatiwa alabadira za. Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

35. Koma ici ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakuchereni msampha, koma kukuthandizani kucita cimene ciyenera, ndi kutsata citsatire Ambuye, opanda coceukitsa.

36. Koma wina akayesa kuti acitira mwana wace wamkazi cosamuyeoera, ngati palikupitirira pa unamwali wace, ndipo kukafunika kutero, acite cimene afuna, sacimwa; akwatitsidwe.

37. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwace, wopanda cikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa cifuniro ca iye yekha, natsimikiza ici mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wace wamkazi, adzacita bwino.

38. Cotero iye amene akwatitsa mwana wace wamkazi acita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa acita koposa.

39. Mkazi amangika pokhala mwamuna wace ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7