Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 4:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

3. Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu, kuti ndiweruzidwe ndi Inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha.

4. Pakuti sindidziwa kanthu kakundiparamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.

5. Cifukwa cace musaweruze kanthu isanadze nthawi yace, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wace wa kwa Mulungu.

6. Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, cifukwa ca inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzace ndi kukana wina.

7. Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli naco ciani cosati wacilandira? Koma ngati wacilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunacilandira?

8. M wadzala kale, mwalemerera kale, mwacita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi mucitadi ufumu, kuti ifenso tikacite ufumu pamodzi ndi inu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 4