Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 5:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anaturuka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nciani ici cirikuturukaci.

6. Ndipo ndinati, Nciani ici? Nati iye, Ici ndi efa alikuturuka. Natinso, Ici ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;

7. (ndipo taonani, cozunguniza cantobvu cotukulidwa) ndipo ici ndi mkazi wokhala pakati pa efa.

8. Ndipo anati, Uyu ndi ucimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntobvu wolemerawo pakamwa pace.

9. Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a cumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo.

10. Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo?

11. Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike, namkhazikeko pa kuzika kwace.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 5