Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 4:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndiwe yani, phiri lalikuru iwe? pamaso pa Zerubabele udzasanduka cidikha; ndipo adzaturutsa mwala wa cimbudzi, ndi kupfuula, Cisomo, cisomo nao.

8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,

9. Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ace omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makatnu anandituma kwa inu.

10. Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona cingwe colungamitsira ciriri m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.

11. Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa coikapo nyali nciani?

12. Ndipo ndinayankha kaciwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zirikutsanula zokha mafuta onga golidi mwa misiwe iwiri yagolidi?

13. Ndipo anandiyankha, nati, Sudziwa kodi kuti nziani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.

14. Pamenepo anati, Awa ndi ana amuna awiri a mafuta oimirira pamaso pa Mbuye wa dziko lonse lapansi.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 4