Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 14:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taonani likudza tsiku la Yehova, limene zofunkha zako zidzagawanika pakati pako.

2. Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mudziwo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mudzi lidzaturuka kumka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mudzimo.

3. Pamenepo Yehova adzaturuka, nadzacita nkhondo ndi amitundu aja, monga anacitira nkhondo tsiku lakudumana.

4. Ndi mapazi ace adzaponda tsiku lomwelo pa phiri la Azitona, liri pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala cigwa cacikuru; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwela.

5. Pamenepo mudzathawa kudzera cigwa ca mapiri anga; pakuti cigwa ca mapiri cidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira cibvomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.

6. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, sikudzakhala kuunika, zowalazo zidzada;

7. koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbe.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 14