Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zefaniya 3:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.

10. Kucokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera naco copereka canga.

11. Tsiku ilo sudzacita manyazi ndi zocita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzacotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzacita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika.

12. Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova.

13. Otsala a Israyeli sadzacita cosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.

14. Yimba, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula, Israyeli; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu.

15. Yehova wacotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israyeli, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso coipa.

16. Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.

17. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi cimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'cikondi cace; adzasekerera nawe ndi kuyimbirapo.

18. Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene katundu wace anawakhalira mtonzo.

19. Taonani, nthawi yomweyo ndidzacita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopitikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale cilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m'dziko lonse.

20. Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi cilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Zefaniya 3