Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zefaniya 3:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Akalonga ace m'kati mwace ndiwo mikango yobangula; oweruza ace ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.

4. Aneneri ace ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza cilamulo.

5. Yehova pakati pace ali wolungama; sadzacita cosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera ciweruzo cace poyera, cosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.

6. Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungondya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo.

7. Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pace pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, nabvunditsa macitidwe ao onse.

Werengani mutu wathunthu Zefaniya 3