Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zefaniya 2:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala husa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta.

7. Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.

8. Ndinamva kutonza kwa Moabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao.

9. Cifukwa cace, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Zedi Moabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pocuruka khwisa ndi maenje a mcere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala amtundu wa anthu anga adzawalandira akhale colowa cao.

10. Ici adzakhala naco m'malo mwa kudzikuza kwao, cifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.

11. Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya pa dziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pace, a m'zisumbu zonse za amitundu.

12. Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.

13. Ndipo adzatambasulira dzanja lace kumpoto nadzaononga Asuri, nadzasanduliza Nineve akhale bwinja, wouma ngati cipululu.

14. Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pace; nyama zonse za mitundu mitundu; ndi bvuo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zace; adzayimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala cipasuko; pakuti anagadamula nchito yace ya mkungudza.

15. Uwu ndi mudzi wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwace, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! wasanduka bwinja, mogonera nyama za kuthengo! yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.

Werengani mutu wathunthu Zefaniya 2