Uwu ndi mudzi wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwace, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! wasanduka bwinja, mogonera nyama za kuthengo! yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.