Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zefaniya 1:15-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi cipasuko, tsiku la mdima ndi la cisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;

16. tsiku la lipenga ndi lakupfuulira midzi yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungondya.

17. Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu a'khungu, popeza anacimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati pfumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.

18. Ngakhale siliva wao, ngakhale golidi wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yace; pakuti adzacita cakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.

Werengani mutu wathunthu Zefaniya 1