Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 9:18-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo ana a Israyeli sanawakantha, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israyeli. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga,

19. Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli, m'mwemo sitikhoza kuwacitira kanthu.

20. Tidzawacitira ici, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo cifukwa ca lumbirolo tidawalumbirira.

21. Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao.

22. Ndipo Yoswa anawaitana, nanena nao, kuti, Mwatinyenga cifukwa ninji, ndi kuti, Tikhala kutaritari ndi inu, pokhala kwanu kuli pakati pa ife?

23. Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.

24. Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wace Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinacita cinthuci.

25. Ndipo tsopano, taonani, tiri m'dzanja lanu; monga muyesa cokoma ndi coyenera kuticitira ife, citani.

26. Pamenepo anawacitira cotero, nawalanditsa m'dzanja la ana a Israyeli, angawaphe.

27. Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 9