Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 7:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma ana a Israyeli analakwa ndi coperekedwaco; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa pfuko la Yuda, anatapa coperekedwaco; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israyeli.

2. Ndipo Yoswa anatuma amuna kucokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Beti-aveni, kum'mawa kwa Beteli; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai.

3. Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka;

4. Potero mwa anthu anakwerako amuna monga zikwi zitatu; koma anathawa pamaso pa amuna a ku Ai.

5. Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapitikitsa kuyambira pacipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.

6. Ndipo Yoswa anang'amba zobvala zace, nagwa nkhope yace pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akulu akulu a Israyeli, nathira pfumbi pamitu pao.

7. Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordano, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordano!

8. Ndidzanenanji, Ambuye, Israyeli atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao?

9. Akadzamva ici Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzacitiranji dzina lanu lalikuru?

10. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako cotere?

11. Israyeli wacimwa, nalakwiranso cipangano canga, ndinawalamuliraco; natengakonso coperekedwaco; anabanso, nanyenganso, naciika pakati pa akatundu ao.

12. Mwa ici ana a Israyeli sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga coperekedwaco, kucicotsa pakati pa inu.

13. Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Pali coperekedwa cionongeke pakati pako, Israyeli iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutacotsa coperekedwaco pakati panu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 7