Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 5:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordano, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku Nyanja ya Mcere anamvakuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordano pamaso pa ana a Israyeli mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo cifukwa ca ana a Israyeli.

2. Nthawi imeneyo Yehova anati kwa Yoswa, Udzisemere mipeni yamiyala, nudulenso ana a Israyeli kaciwiri.

3. Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israyeli pa Gibeya Naraloti.

4. Koma cifukwa cakuti Yoswa anawadula ndi ici: anthu onse oturuka m'Aigupto, anthu amuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'cipululu panjira, ataturuka m'Aigupto.

5. Pakuti anthu onse anaturukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m'cipululu panjira poturuka m'Aigupto sanadulidwa.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 5